Kodi ndingakwaniritse bwanji zofunikira kuti ndipeze gulu lapamwamba la Deriv P2P?
Kuti mupite pa gulu (tier) lapamwamba la P2P, muyenera kukwaniritsa zofunikira za kuchita malonda ndi mmene mwachitira bwino.
Gulu lililonse limadalira izi:
- Nthawi pa pulatifomu – Kutalika kwa nthawi yomwe mwakhala mukugwiritsa ntchito Deriv P2P
- Kuchita malonda – Kuchuluka konse kwa malonda anu a P2P
- Mbiri ya mikangano – Chiwerengero cha mikangano yomwe inu ndinu olakwa m'masiku 30 apitawa
- Muyeso wa kumaliza malonda – Peresenti ya maodala omwe amalizidwa bwino
Kukwaniritsa zofunikira izi kumatsegula magulu apamwamba okhala ndi malire okwera a malonda.






