Nsanja yochitira malonda ya DBot
Mu phunziro lomaliza la maphunziro ano tiona za Deriv Bot, njira yamphamvu yosafuna kulemba code yomwe imakulolani kupanga njira zamalonda zodziyendetsa zokha mosavuta ndikugwiritsa ntchito mwayi wamalonda maola 24 pa tsiku, masiku 7 pa sabata (24/7). Pogwiritsa ntchito njira yosavuta yokoka ndi kuika “mabuloko”, ochita malonda a luso lililonse akhoza kupanga njira zawozawo zomwe zimagwirizana ndi zosowa zawo zamalonda.
Chiyambi cha Deriv Bot
Deriv Bot idapangidwa kuti ikhale yosavuta kugwiritsa ntchito, kupereka mawonekedwe omveka bwino kwa ochita malonda kuti aziyendetsa njira zawo zamalonda zokha popanda kufunikira luso lolemba mapulogalamu.
Kupeza Deriv Bot
Kuti muyambe kugwiritsa ntchito Deriv Bot:
- Lowani mu akaunti yanu pa Trader's Hub ya Deriv.
- Sankhani “Deriv Bot” pa zosankha zomwe zilipo kuti mulowe pa Dashboard ya Bot.
Mukalowa, mudzaona zosankha zingapo zoyambira ulendo wanu wamalonda.
Zinthu Zopezeka pa Dashboard ya Deriv Bot
Mukalowa pa Dashboard ya Deriv Bot, mudzaona zosankha zazikulu zinayi:
- Tsegulani Njira Zomwe Zilipo Kale:itanitsani njira kuchokera pa “My Computer” kapena “Google Drive.”
- Njira Yachangu: Njira yofulumira kwambiri yoyambitsira bot yamalonda pogwiritsa ntchito zitsanzo za njira zokonzedweratu.
- Chomangira Bot: Kwa ogwiritsa ntchito akatswiri, izi zimawalola kupanga njira zawozawo kuyambira pachiyambi.
Njira Yachangu
Mbali ya Njira Yachangu imagawa bot iliyonse yamalonda m'magawo awiri akuluakulu:
- Chitsanzo cha Njira: Ichi chimatsimikizira momwe bot yanu idzasinthire kuchuluka kwa Stake pambuyo pa malonda aliwonse kutengera phindu.
- Zitsanzo za Njira zikuphatikizapo:
- Martingale: Imawirikiza kawiri Stake mukaluza kuti mubwezeretse ndalama zomwe zatha.
- D'Alembert: Imasintha Stake molingana ndi mlingo wokhazikitsidwa, kuionjezera mukaluza ndikuichepetsa mukapeza phindu.
- Oscar's Grind: Imaika chidwi pa kupeza phindu laling'ono komanso lokhazikika.
- Reverse Martingale: Imaonjezera Stake mukapeza phindu ndikuichepetsa mukaluza kuti mukulitse phindu lotsatizana.
- 1-3-2-6: Imatsatira ndondomeko yokhazikika ya Stake pakapezeka phindu lotsatizana.
- Martingale: Imawirikiza kawiri Stake mukaluza kuti mubwezeretse ndalama zomwe zatha.
- Zitsanzo za Njira zikuphatikizapo:
- Zokonda pa Malonda: Zokonda izi zimafotokoza chinthu chomwe chidzagulitsidwe, mtundu wa malonda, zofunikira pogula, Stake yoyambirira, nthawi, mlingo wa phindu, komanso mlingo wa kuluza.
Kukonza Njira Yanu
Mukasankha chitsanzo cha njira yanu ndikudzaza zokonda pa malonda zomwe zikufunika, ingodinani “Run” kuti muyambitse bot yanu. Onetsetsani kuti mwayesererapo njira iliyonse pa akaunti yoyeserera (demo) choyamba kuti mukonze bwino kakonzedwe kanu ndikukhala ndi chidaliro.
Kugwiritsa Ntchito Chomangira Bot
Kwa iwo amene akufuna kusintha njira zawo mozama, Chomangira Bot chimapereka mbali zapamwamba izi:
- Malo Ogwirira Ntchito (Canvas): Apa ndi pamene mumakoka ndikuika mabuloko kuti mupange ntchito zapadera za bot yanu.
- Mndandanda wa Mabuloko: Wogawidwa m'magulu a zokonda pa malonda, zofunikira pogula, zofunikira pogulitsa, ndi zofunikira poyambitsanso malonda. Buloko iliyonse ili ndi malangizo apadera omwe amatsogolera momwe bot imagwirira ntchito.
Zitsanzo za Ntchito za Mabuloko
- Zokonda pa Malonda: Fotokozani msika womwe mukufuna kuchitira malonda, mitundu ya makontrakiti, ndi kuchuluka kwa Stake.
- Zofunikira Pogula: Fotokozani nthawi yomwe bot iyenera kulowa mu malonda kutengera zomwe mwakhazikitsa.
- Zofunikira Pogulitsa: Perekani malangizo amomwe bot iyenera kuchitira pamene malonda ali mkati.
- Zofunikira Poyambitsanso Malonda: Khazikitsani zomwe zimachitika kontrakiti ikatha musanayambe ina yatsopano.
Mathero
Ndi Deriv Bot, muli ndi chida champhamvu pamanja panu chopangira njira zamalonda zodziyendetsa zokha zomwe zimagwirizana ndi kalembedwe komanso zokonda zanu zamalonda. Pogwiritsa ntchito Njira Yachangu komanso Chomangira Bot, mukhoza kukhazikitsa dongosolo lolongosoka lochitira malonda pa nsanja ya Deriv.
Kumbukirani kuyeserera mokwanira pa akaunti yoyeserera (demo) kuti mutsimikizire kuti mukumvetsa bwino tsatanetsatane wa njira zomwe mwasankha musanayambe kuchita malonda enieni. Mu phunziro lathu lotsatira, tidzaona kagwiritsidwe ntchito ka njira zamalonda pa zinthu za Synthetic za Deriv pogwiritsa ntchito Options. Zikomo pokhala nafe mu phunziro lino, ndipo tikufunirani malonda abwino!
Quiz
Kodi ubwino waukulu wogwiritsa ntchito Deriv Bot ndi chiyani?
Kodi njira ya Martingale imaphatikiza chiyani?
Ndi mbali iti yomwe imalola kusintha mwapamwamba njira zamalonda mu Deriv Bot?


