
Kulowa mu malonda osayeserera kuli ngati kuyendetsa galimoto pamsewu waukulu wodzaza magalimoto kwa nthawi yoyamba: N'koopsa komanso kododometsa.. Apa ndipamene akaunti yoyesera malonda (demo) imathandizira! Ndi njira yanu yoyesera malonda, yomwe imakulolani kufufuza misika, kuyesa njira njira zamalonda, komanso kuzolowera zida zamalonda—zonsezi popanda kuika pachiwopsezo kasamalidwe ka chiwopsezo ngakhale kobiri limodzi la ndalama zenizeni.
Kodi akaunti yoyesera malonda (demo) n'chiyani, ndipo n'chifukwa chiyani ili yofunika?
Akaunti yoyesera malonda (demo) ndi njira yaulere komanso yopanda chiwopsezo yophunzirira mmene malonda amagwirira ntchito. Imakupatsani mwayi woona mmene msika weniweni umakhalira, kukulolani kuyeserera njira zosiyanasiyana pogwiritsa ntchito ndalama zongoyerekeza. Ganizirani izi ngati chipangizo chophunzirira kuyendetsa ndege kwa amalonda—mumapeza chidziwitso chonse popanda chiwopsezo chotaya ndalama zenizeni.
Kodi mungatsegule kuti akaunti yoyesera malonda (demo)?
Deriv imapereka maakaunti oyesera (demo) pa mapulatifomu ake onse amalonda, omwe amakhala ndi USD 10,000 za ndalama zongoyerekeza. Mutha kuwonjezera Ndalama Zotsala nthawi iliyonse ndikufufuza misika yosiyanasiyana, kuyambira Forex mpaka Masheya, Ndalama za Crypto, komanso Synthetic Indices.
Kuyeserera malonda osagwiritsa ntchito ndalama zenizeni

Amalonda ena amathamangira kulowa mu malonda enieni posachedwa kwambiri, kufunafuna phindu lalikulu opanda chidziwitso. Zimenezi nthawi zambiri zimabweretsa kutayika kopweteka. Akaunti yoyesera (demo) imakulolani kuyesa njira, kumvetsetsa zida za kasamalidwe ka chiwopsezo, ndikulimbitsa chidaliro popanda kutaya ndalama zenizeni.
Pa Deriv Trader, mutha kuyeserera malonda a Options ndikufufuza Multipliers, zomwe zili ndi zida zosamalira chiwopsezo monga Stop Loss, Take Profit, ndi kuthetsa malonda (deal cancellation).
Kugwiritsa ntchito maakaunti oyesera (demo) popenda msika
Misika imasintha kutengera mmene zinthu zikuyendera, zochitika zapadziko lonse, komanso khalidwe la ogula ndi ogulitsa pamsika. Kumvetsetsa kusinthaku n'kofunika kwambiri. Ndi akaunti yoyesera (demo), mutha kuphunzira mmene msika ulili panthawi yeniyeni, kuyesa zida zowunikira malonda (technical analysis), ndikupanga njira zamalonda popanda mantha otaya ndalama.
Deriv MT5 (DMT5) ndi pulatifomu yabwino kwambiri yochitira izi. Imapereka zida zapamwamba za matchati, zizindikiro (indicators), ndi mbali zowunikira zokuthandizani kupeza chidziwitso chonse cha malonda musanagwiritse ntchito akaunti yeniyeni.
Kupanga ndondomeko yamalonda musanayambe malonda enieni
Wamalonda wabwino sachita malonda mwachisawawa. Kupanga ndondomeko yoyenera yamalonda kumakuthandizani kukhala odziletsa. Ndi akaunti yoyesera (demo), mutha:
- Kukhazikitsa zolinga zotheka ndikusankha kalembedwe kamalonda kamene kamakuyenererani (scalping, swing trading).
- Kufotokoza njira zolowera ndi zotulukira mu malonda pogwiritsa ntchito zizindikiro zowunikira (technical indicators).
- Kuyeserera kasamalidwe ka chiwopsezo pogwiritsa ntchito malamulo a Stop Loss ndi kuyeza kukula kwa malonda.
Kodi muyenera kusinthira liti ku akaunti yeniyeni?
Palibe yankho limodzi lokha kwa aliyense, koma izi ndi zizindikiro zina zosonyeza kuti mwina mwakonzeka:
- Mwayesa njira yamalonda bwinobwino (kupeza phindu pa malonda oposa 50% amene mwachita).
- Mumasamalira bwino ndalama zanu komanso mumamvetsetsa kasamalidwe ka chiwopsezo.
- Mutha kuchita malonda osalola kuti malingaliro ndi zakukhosi kwanu zilamulire zisankho zanu.
Quiz
Kodi ubwino waukulu wa akaunti yoyesera malonda ndi chiyani?


