Kusankha mlingo woyenera wa kusinthasintha kwa mitengo
Pamalonda, kusinthasintha kwa mitengo kumatanthauza mlingo umene mtengo wa chinthu umasinthira pa nthawi inayake. Ndi chizindikiro chofunikira kwambiri cha mayendedwe a msika komanso chinthu chachikulu powunika chiopsezo. Kusinthasintha kwakukulu kumatanthauza kuti mtengo wa chinthu ukhoza kusintha kwambiri pa nthawi yochepa, zomwe zingabweretse phindu lalikulu kapena kutayika kwakukulu. Mosiyana ndi zimenezi, kusinthasintha kochepa kumasonyeza kukhazikika kwa mitengo popanda kusintha kwadzidzidzi. Kumvetsetsa kusinthasintha kwa mitengo n'kofunika kwambiri kuti muyendetse komanso kuchita malonda mogwira mtima m'misika.
Ma Volatility Indices amaimira milingo yosiyanasiyana imeneyi ya kusintha kwa mitengo ndipo amapangidwa kuti agwirizane ndi njira zosiyanasiyana zamalonda. Phunziroli likupatsani chidziwitso pa makhalidwe a ma Volatility Indices, zoyenera kuganizira kwa ochita malonda, komanso njira zothandiza pochita malonda mogwira mtima.
Makhalidwe a ma Volatility Indices
Deriv imapereka ma Volatility Indices osiyanasiyana, ndipo iliyonse imadziwika ndi peresenti yake ya kusinthasintha yomwe imatsimikizira kusintha kwa mitengo komwe kukuyembekezeka. Ngakhale kuti ma Volatility Indices wamba amakhala ndi kusintha kwa mtengo (Tick) masekondi awiri aliwonse, Deriv imaperekanso ma index omwe ali ndi mlingo womwewo wa kusinthasintha, koma okhala ndi Tick yomwe imachitika sekondi iliyonse. Mutha kuzindikira ma index amenewa ndi chizindikiro cha (1s) chomwe chili pa dzina lake.
Pansipa pali zitsanzo zingapo zodziwika bwino, ndipo mlingo wawo wa kusinthasintha wafotokozedwa mwatsatanetsatane:
- Volatility 10 Index: Ndi kusinthasintha kwa 10%, index imeneyi n'oyenera kwa ochita malonda omwe akufuna kukhazikika komanso kusintha kochepa kwa mitengo, zomwe zimaipangitsa kukhala yabwino kwambiri kwa oyamba kumene kapena amene amakonda malo amalonda odziwikiratu.
- Volatility 25 Index: Popeza imapereka kusintha kokwerako pang'ono poyerekeza ndi 10 Index, Volatility 25 Index imabweretsa kugwirizana pakati pa chiopsezo ndi phindu. Imalola ochita malonda kuona mayendedwe ochulukirapo uku akusungabe mlingo winawake wa kukhazikika.
- Volatility 100 Index: Index imeneyi ili ndi kusinthasintha kwa 100%, komwe kumaimira msika wosadziwikiratu bwino. Imapereka mwayi wopeza phindu lalikulu, koma ziopsezo zomwe zimayendera nazo zimaipangitsa kukhala yoyenera kwa ochita malonda odziwa bwino ntchitoyi omwe angathe kuyendetsa njira zamalonda zozama.
- Volatility 150 Index: Pokhala ndi kusinthasintha kwakukulu kwambiri pa 150%, index imeneyi n'oyenera kwa ochita malonda omwe amachita bwino m'malo achiwopsezo komanso othamanga kwambiri. Ngakhale kuti imapereka mipata yopezera phindu lalikulu, imabweranso ndi chiopsezo chotaya ndalama zambiri, choncho pamafunika njira zolimba zochepetsera chiopsezo.




Kuwunika Njira Yanu Yamalonda ndi Mlingo Wopirira Chiopsezo
Posankha Volatility Index, n'kofunika kuganizira njira yanu yochitira malonda komanso mlingo wanu wopirira chiopsezo:
- Mlingo Wopirira Chiopsezo: Kodi mumakhala omasuka ndi kusintha kwadzidzidzi kwa mitengo, kapena mumakonda mayendedwe odziwikiratu? Mlingo wanu wopirira chiopsezo udzakhudza kwambiri chisankho chanu cha index.
- Chidziwitso Pamalonda: Oyamba kumene angaone kuti n'kothandiza kuyamba ndi ma index omwe ali ndi kusinthasintha kochepa, monga Volatility 10 Index, kuti azolowere mayendedwe a msika. Kumbali ina, ochita malonda odziwa bwino ntchitoyi akhoza kusankha ma Volatility 75 kapena 100 Indices omwe amasinthasintha kwambiri, pofuna kupeza phindu lalikulu.
- Maganizo Okonzekera: Wunikani kuchuluka kwa nthawi ndi khama lomwe mwakonzeka kupereka poyang'anira ndi kusanthula malonda. Ma index osinthasintha kwambiri angafune chidwi chochuluka komanso kupanga zisankho mwachangu, pomwe ma index osinthasintha pang'ono angalole njira yodekha yochitira malonda.
Njira Zothandiza Zamalonda pa ma Volatility Indices
Volatility Index iliyonse imagwirizana ndi njira zosiyanasiyana zamalonda kutengera makhalidwe ake a kusinthasintha, koma izi ndi zina mwa njira zabwino kwa amene akufuna kuchita malonda a ma Volatility Indices:
- Kugwiritsa Ntchito Malamulo a Stop Loss: M'misika yosinthasintha kwambiri monga Volatility 75 kapena 100, ndi chizolowezi chabwino kugwiritsa ntchito malamulo a Stop Loss. Chida chimenechi chimathandiza kuchepetsa kutayika komwe kungachitike potseka malonda okha akafika pa mtengo winawake.
- Kutsatira Mayendedwe a Msika: Pa ma index monga Volatility 50 ndi 100, ganizirani zogwiritsa ntchito njira yotsatira mayendedwe a msika. Izi zimaphatikizapo kusanthula mayendedwe a msika kuti muzindikire mbali imene msika ukupita ndikuyika malonda kutsatira mbali imeneyo.
- Kugawa Malonda: Kugawa malonda anu m'ma Volatility Indices angapo kungathandize kuchepetsa chiopsezo. Mwachitsanzo, kukhala ndi malonda mu Volatility 10 Index komanso mu Volatility 150 Index kumakulolani kufanizira chiopsezo uku mukugwiritsa ntchito milingo yosiyanasiyana ya mayendedwe a msika.
Quiz
Kodi kusinthasintha kwa mitengo kumatanthauzidwa bwanji pankhani za malonda?
Ndi chizindikiro chiti chimene chimapangitsa Volatility 10 Index kukhala yoyenera kwa amalonda osamala?
N'chifukwa chiyani ochita malonda ayenera kugwiritsa ntchito malamulo a Stop Loss m'misika yosakhazikika?


