
Ma Vanilla Options, omwenso amadziwika kuti “vanillas”, ndi njira yabwino kwambiri yochitira malonda m'misika mosinthasintha pochita malonda a Options. Amakupatsani ufulu (koma osati kukakamizidwa) wogula kapena kugulitsa chuma pamitengo yoikika tsiku linalake lisanafike. Zikumveka zovuta? Tiyeni tifotokoze pang'onopang'ono.
Kodi ma Vanilla Options amagwira bwanji ntchito?
Kugula Vanilla Option kuli ngati kupeza chiphaso chololedwa kulowa kuseri kwa siteji. Mumalipirira mwaiwo koma n'kusankha ngati mugwiritse ntchito kapena ayi. Ngati zinthu zikuyenda bwino (msika ukuyenda mokukomerani), mutha kugwiritsa ntchito chiphaso chanu ndikusangalala ndi phindu lake. Ngati sichoncho, choipa chachikulu chomwe chingachitike n'chakuti mwataya mtengo wa chiphasocho basi, palibenso china.
Mawu ofunikira kuwadziwa
Musanayambe, nayi mawu ofunikira omwe muyenera kuwadziwa:
- Tsiku lotha ntchito: Tsiku lomaliza la option yanu. Tsiku ili likadutsa, chiphaso chanu (option) chimatha ntchito ndipo sichingagwiritsidwenso ntchito.
- Ndalama ya Stake: Mukagula Vanilla Option, mumalipira ndalama yotchedwa premium kapena ndalama ya Stake kwa wogulitsa option. Premium iyi imakhala ngati mtengo wopezera ufulu womwe mgwirizano wa option umapereka.
- Call option: Imakulolani kugula chuma pa mtengo woikika (strike price) isanathe ntchito, ndipo ndi yabwino ngati mukuganiza kuti mitengo ikwera.
- Put option: Imakulolani kugulitsa chuma pa mtengo woikika (strike price) isanathe ntchito, ndipo ndi yothandiza ngati mukuganiza kuti mitengo itsika.
ndi Deriv, migwirizano iyi imalipiridwa ngati Payout m'malo mwa chuma chenichenicho.
- Phindu lenileni (Intrinsic value): Kusiyana komwe kulipo pakati pa mtengo wamakono wa chuma ndi mtengo woikika (strike price).
- Phindu la nthawi (Time value): Limasonyeza nthawi yomwe yatsala isanathe ntchito, nthawi yochuluka nthawi zambiri imatanthauza phindu lochuluka.
- Mtengo woikika (Strike price): Mtengo woikika (strike price), womwenso umadziwika kuti exercise price, ndi mfundo yofunika kwambiri pa malonda a Options. Umaimira mtengo wokhazikitsidwa kale womwe mwiniwake wa option angagulire (ngati ili call option) kapena kugulitsira (ngati ili put option) chuma chake. Mtengo woikika umakhazikitsidwa pamene mgwirizano wa option ukupangidwa ndipo umagwira ntchito yofunika kwambiri podziwa Payout yomwe option ingapereke.
Chifukwa chiyani muyenera kuchita malonda a Vanilla Options?
amalonda amakonda ma Vanilla Options chifukwa amapereka kusinthasintha komanso mwai wopeza phindu. Umu ndi momwe mungawagwiritsire ntchito:
- Mukuyembekezera kuti mtengo wa chuma ukwera? Gulani call option kuti mutseke mtengo wotsika wogulira. Izi zikutanthauza kuti ngakhale mtengo wamsika utakwera kuposa mtengo wanu woikika (strike price), mukadali ndi ufulu wogula pa mtengo woikika womwe munagwirizana.

- Mukuganiza kuti mitengo itsika? Gulani put option kuti muthe kugulitsa pa mtengo wokwera. Izi zikutanthauza kuti ngakhale mtengo wamsika utatsika pansi pa mtengo wanu woikika (strike price), mukadali ndi ufulu wogulitsa pa mtengo woikika womwe munagwirizana.

Inde, palibe malonda opanda chiopsezo. Ngakhale ma Vanilla Options angakhale osangalatsa, nthawi zonse ndi bwino kusamalira chiopsezo chanu ndikuchita malonda mosamala.
Yambani molimba mtima kuyamba kuchita malonda
Ma Vanilla Options amakupatsani njira zambiri zochitira malonda, koma ngati chida china chilichonse chachuma, amabwera ndi ziopsezo. Ngati ndinu watsopano pa malonda a Options, bwanji osayamba ndi akaunti yoyeserera (demo) pa Deriv? Muthanso kukulitsa luso lanu ndi maphunziro aulere pa Deriv Academy.
Mwakonzeka kuyamba?
Lowani mu Deriv Academy pogwiritsa ntchito imelo ndi mawu achinsinsi a akaunti yanu ya Deriv yomwe mulinayo kale.
Yeserani ndi akaunti yoyeserera (demo) ndikuchita malonda mosamala.
Quiz
Ndi chiganizo chiti mwa izi chokhudza ma Vanilla options chomwe chili choona?


