
Kodi mukuganizira zochita malonda a Contract for Difference (CFDs) koma simukudziwa komwe mungayambire? Tiyeni tikambirane za Deriv MT5, nsanja yodalirika yochitira malonda a ma CFD mwachangu. Kaya ndinu oyamba kumene kapena wamalonda wodziwa bwino ntchitoyi, Deriv MT5 ili ndi zonse zomwe mukufunikira kuti muchite malonda mwachidziwitso.
Kodi malonda a CFD n'chiyani kwenikweni?
Ndi ma CFDs, simukhala eni ake a katundu ngati golide kapena masheya. M'malo mwake, mumaneneratu ngati mtengo wake udzakwera kapena kutsika. Ngati mwaneneratu molondola, mumapeza phindu. Ngati sichoncho, muthauluza ndalama. N'zosavuta, sichoncho? Deriv MT5 imapangitsa malonda a CFD kukhala osavuta komanso oyenda bwino.
Chifukwa chiyani muyenera kuchita malonda ndi Deriv MT5?
Deriv MT5 si nsanja chabe ina yochitira malonda yopangidwa kuti ikupangitseni moyo kukhala wosavuta. Nazi zifukwa zomwe amalonda amayikondera:
- Yosavuta kugwiritsa ntchito: Kaya ndinu atsopano kapena odziwa bwino malonda, chilichonse n'chosavuta kuchipeza ndi kuchigwiritsa ntchito.
- Chidziwitso cha msika: Ma chati ndi zipangizo zimakuthandizani kulondoloza mayendedwe a msika komanso kupeza mipata yochitira malonda.
- Zosankha zambiri: Chitani malonda a ndalama za maiko, Commodities, masheya, komanso Derived Indices yapadera ya Deriv.
- Ma akaunti ogwirizana ndi zofuna zanu: Mitundu yosiyanasiyana ya ma akaunti imagwirizana ndi njira zosiyanasiyana zochitira malonda komanso milingo ya luso lanu.
Pezani akaunti yoyenera kwambiri kwa inu
Deriv MT5 imapereka mitundu yambiri ya ma akaunti kuti igwirizane ndi zosowa zosiyanasiyana za malonda:
- Akaunti ya Standard. Ndi yabwino pazinthu zonse ndipo ili ndi Spreads zotsika mtengo komanso malipiro a swap abwino.
- Akaunti ya Swap-free. Palibe malipiro osungira malonda usiku wonse, ndipo ndi yabwino kwambiri kwa amalonda anthawi yayitali.
- Akaunti ya Zero spread. Palibe Spreads, pali ma Commission okhazikika okha omwe amakupatsani mitengo yolondola komanso yodziwika bwino.
- Akaunti ya Financial. Ili ndi Spreads zochepa kwambiri kwa omwe amachita malonda pafupipafupi.
Kodi mumagwiritsa ntchito pati Deriv MT5: Pa kompyuta, pa intaneti, kapena pa foni?
Ziribe kanthu momwe mumakondera kuchita malonda, pali mtundu wa Deriv MT5 womwe umagwirizana ndi kalembedwe kanu:
Pulogalamu ya pa kompyuta (Desktop terminal). Njira yokhala ndi mbali zonse za pa Windows, macOS, ndi Linux.
- Yang'anirani ma chati angapo nthawi imodzi.
- Gwiritsani ntchito zizindikiro zaukadaulo ndi zipangizo zojambulira kuti muwunike mayendedwe a msika.
- Yang'anirani mitengo ya katundu pogwiritsa ntchito Market Watch.
- Chitani malonda odziyendetsa okha ndi ma Expert Advisors (EAs).
Deriv MT5 pa intaneti. Palibe kutsitsa pulogalamu, mumangolowa mwachangu kudzera pa msakatuli (browser) wanu.
- Chitani malonda kuchokera kulikonse, nthawi iliyonse.
- Maonekedwe osavuta komanso omveka bwino.
- Nthawi zonse imakhala ndi mbali zatsopano zamakono.
Deriv MT5 pa foni. Chitani malonda molimba mtima popita paliponse.
- Landirani zosintha za msika pompopompo.
- Yendetsani malonda anu nthawi yomweyo pa chipangizo chanu.
- Khalani olumikizika kulikonse komwe mungapite.
Kodi mwakonzeka kuyamba kuchita malonda?
Kuyamba kugwiritsa ntchito Deriv MT5 n'kosavuta. Ingopitani pa webusayiti ya Deriv, tsitsani mtundu womwe ukukuyenererani bwino, kapena yesani ya pa intaneti kuti muyambe mopanda zovuta. Ngati ndinu atsopano, yeserani kaye pa akaunti yoyesera (demo) musanayambe kuchita malonda ndi ndalama zenizeni.
Kodi mukufuna kuphunzira zambiri? Fufuzani maphunziro aulere a Deriv MT5 kuti mulimbikitse chidaliro chanu.
Quiz
Ngati mukufuna mbali zapamwamba kwambiri, muyenera kusankha mtundu uti?


