
Ma Fibonacci retracement amagwiritsidwa ntchito kwambiri pozindikira malo omwe msika ungatembenukire pa kuwunika kwa luso la malonda. Amathandiza kuzindikira malo ofunikira a support ndi resistance pogwiritsa ntchito malo a support ndi resistance osavuta komanso ma chiŵerengero a masamu odziwika bwino. Umu ndi mmene amagwirira ntchito. Sikufunika masamu ovuta.
Nanga nkhani ya manambala a Fibonacci n'chiyani?
Manambala a Fibonacci ndi ndandanda ya masamu yomwe nambala iliyonse imakhala kuphatikiza kwa manambala awiri omwe ali patsogolo pake. Mwachitsanzo: 0, 1, 1, 2, 3, 5, 8, 13, 21… ndi zina zotero.
Dongosolo limeneli limaonekera paliponse m'chilengedwe: kuyambira pa kuzungulira kwa nkhono za m'nyanja mpaka mmene mbeu za mpendadzuwa zimayalidwira. Miyezo imeneyi imaonekeranso pa kayendedwe ka mitengo ya pamsika — kulondola kochititsa chidwi pantchito.
Mmene migawo ya Fibonacci retracement imagwirira ntchito
Chida cha Fibonacci retracement chimapanga mizere yopingasa pa ma peresenti ofunikira potengera kusuntha kwa mtengo, zomwe zimathandiza kulosera malo a support kapena resistance. Migawo yofunikira imeneyi ndi:
- 0% (poyambira pa kayendedwe ka mtengo)
- 23.6%
- 38.2%
- 50% (si nambala yeniyeni ya Fibonacci, koma amalonda amaiikonda)
- 61.8% (chiŵerengero cha golide, chomwe chimadziwikanso kuti nambala yamatsenga)
- 78.6%
- 100% (mapeto a kayendedwe ka mtengo)
Umu ndi mmene mungazigwiritsire ntchito kwenikweni. Pezani kusuntha kwakukulu kwa mtengo (kukwera kapena kutsika), ndipo migawo ya retracement ikuthandizani kulosera komwe mtengo ungayime pang'ono kapena kubwerera m'mbuyo.

Kuona migawo ya Fibonacci ikugwira ntchito
Tiyerekeze kuti mtengo wa katundu wakwera mwachangu kuchoka pa $100 kufika pa $200. Ngati ubwerera m'mbuyo pang'ono, mungayembekezere support pafupi ndi migawo yofunikira ya Fibonacci. Mwachitsanzo, kubwerera m'mbuyo kwa 50% kumatanthauza kuti mtengo ungatsike kufika pa $150 usanayambe kukweranso.
Migawo yosiyanasiyana imatanthauza zinthu zosiyanasiyana:
- 23.6% - 38.2%: Kubwerera m'mbuyo kwapang'ono, nthawi zambiri mu kayendedwe ka mtengo kolimba.
- 50% - 61.8%: Malo ofunikira komwe mtengo umakonda kuyima kapena kutembenuka.
- 78.6% - 100%: Kubwerera m'mbuyo kwakukulu komwe kuli ndi malo oti mtengo ungatembenukire.

Mmene mungagwiritsire ntchito ma Fibonacci retracement pamalonda
Mutha kupeza zida za Fibonacci mwachindunji mu Deriv MT5 pansi pa Insert

Njira zogwiritsira ntchito migawo ya Fibonacci retracement:
- Limodzi ndi support/resistance: Ngati mugawo wa Fibonacci ukugwirizana ndi pamwamba kapena pansi pa m'mbuyomu, malowo amakhala ofunikira kwambiri.
- Limodzi ndi ma moving average: Kubwerera m'mbuyo kufika pa moving average (monga 50-day MA) kungatsimikizire kutembenuka kwa mtengo.
- Limodzi ndi mitundu ya ma candlestick: Kodi pali bullish engulfing candle pafupi ndi mugawo wa 61.8%? Chimenecho n'chizindikiro champhamvu.
- Pa ma timeframe osiyanasiyana: Chepetsani kukula kwa tchati kuti muone migawo ikuluikulu yomwe amalonda akuluakulu angakhale akuiyang'anira.
- Limodzi ndi RSI kapena Stochastics: Kodi zagulitsidwa mopitirira muyeso (oversold) pamugawo wofunikira wa Fibonacci? Chimenecho chingakhale chizindikiro chogula.
Quiz
Sheya yakwera kuchoka pa $50 kufika pa $100. Kodi mlingo wa 50% retracement uli pati?


