
Chifukwa chake deta yachuma ilili yofunika
Ngati mwangoyamba kumene malonda a Forex, mungafunse chifukwa chake amalonda odziwa bwino ntchitoyi amayang'anitsitsa makalenda achuma komanso nkhani zomwe zimatuluka. Chifukwa chake n'chosavuta: ndalama zimayimira chuma cha mayiko, ndipo deta yachuma imafotokoza momwe chuma chomwecho chikuyendera. Ganizirani zizindikiro zachuma ngati zipangizo zoyesera mphamvu ya chuma. Zimathandiza amalonda kuneneratu kuti ndi ndalama ziti zomwe zingakwere mphamvu kapena kuchepa mphamvu.
Zizindikiro zazikulu zachuma zomwe zimakhudza misika ya Forex
Chuma chonse chopangidwa m'dziko (GDP)
GDP imayesa zonse zomwe dziko limapanga, kuyambira katundu mpaka ntchito. Kukwera kwa GDP nthawi zambiri kumalimbitsa ndalama ya dziko, pomwe kuchepa kwa GDP kungayifooketse. Mwachitsanzo, ngati GDP ya dziko la UK iposa zomwe zimayembekezeredwa, ndalama ya British pound ingakwere mphamvu poyerekeza ndi ndalama zina.
Deta ya msika wantchito
Deta yokhudza ntchito nthawi zambiri imakhudza kwambiri mphamvu ya ndalama. Ku US, zizindikiro zazikulu za msika wantchito zikuphatikizapo:
- Chiwerengero cha kusowa kwa ntchito. Gawo la pa zana la anthu omwe alibe ntchito pagulu la anthu otha kugwira ntchito.
- Avareji ya malipiro a pa ola. Muyeso wa kukula kwa malipiro, womwe umakhudza kagwiritsidwe ntchito ka ndalama ka ogula.
- Ntchito zopanda ulimi (NFP). Chiwerengero cha ntchito zatsopano zomwe zawonjezedwa, kupatulapo ntchito za ulimi.
Malipoti antchito abwino kuposa momwe amayembekezeredwa nthawi zambiri amakweza mphamvu ya ndalama, pomwe ziwerengero zochepa zingachititse kuti itsike.
Ziwongoladzanja ndi zisankho za Mabanki Akuluakulu
Mabanki akuluakulu, monga Federal Reserve, European Central Bank, kapena Bank of England, amakhazikitsa ziwongoladzanja, zomwe zimakhudza mphamvu ya ndalama. Ziwongoladzanja zokwera nthawi zambiri zimakopa ochita malonda akunja, zomwe zimalimbitsa ndalamayo.
Zinthu zazikulu zofunika kuziyang'anira:
- Chisankho chenicheni cha chiwongoladzanja poyerekeza ndi zomwe msika umayembekezera.
- Zolozera za mtsogolo (zizindikiro zokhudza kusintha kwa chiwongoladzanja mtsogolo).
- Kalankhulidwe ka zikalata zotsagana nazo (kalankhulidwe kokhwima 'hawkish' = kuthekera kokweza chiwongoladzanja, kalankhulidwe kofewa 'dovish' = kuthekera kotsitsa chiwongoladzanja).
Miyeso ya kukwera kwa mitengo ya zinthu
Kukwera kwa mitengo ya zinthu kumathandiza kwambiri pa zisankho za chiwongoladzanja. Chiwerengero cha Mitengo ya Zinthu Zogula (CPI) chimatsatira kusintha kwa mitengo pakapita nthawi. Mabanki akuluakulu nthawi zambiri amalingalira kuti kukwera kwa mitengo ya zinthu kukhale pafupifupi 2%. Kukwera kwambiri kwa mitengo kungabweretse kukwezedwa kwa chiwongoladzanja, zomwe zimalimbitsa ndalama, pomwe kutsika kwa mitengo kungachititse kuti chiwongoladzanja chichepetsedwe.
Kusiyana kwa malonda akunja
Muyeso uwu umayerekeza katundu amene dziko limatumiza kunja ndi amene limayitanitsa kuchokera kunja:
- Phindu la malonda akunja (kutumiza katundu wambiri kunja kuposa kuyitanitsa) → Kumalimbitsa ndalama.
- Kuchepa kwa malonda akunja (kuyitanitsa katundu wambiri kuchokera kunja kuposa kutumiza) → Kumafooketsa ndalama.
Momwe nkhani zimayendetsera kusintha kwa msika
Zilengezo za mabanki akuluakulu
Izi ndi zina mwa zinthu zazikulu kwambiri zomwe zimasuntha msika. Misika imachita chidwi ndi:
- Kusintha kwa ziwongoladzanja.
- Zosintha pa ndondomeko zogulira ma bondi.
- Kusintha pa zoneneratu zachuma.
- Zikalata za ndondomeko.
Ngakhale kusintha kwakung'ono pa kalankhulidwe kungayambitse kusuntha kwakukulu kwa ndalama.
Kutuluka kwa deta yachuma
- Deta yabwino kuposa momwe imayembekezeredwa → Nthawi zambiri imalimbitsa ndalama.
- Deta yochepa mphamvu kuposa momwe imayembekezeredwa → Nthawi zambiri imafooketsa ndalama.
- Kukula kwa zodabwitsa pa detayo, kumakulitsanso kusuntha kwa msika.
Zochitika zandale komanso za mayiko
Zochitika zazikulu zandale zingakhale ndi zotsatira za nthawi yayitali pa misika ya ndalama:
- Zisankho
- Ma referendamu onga Brexit
- Mgwirizano kapena mikangano yamalonda
- Mikangano ya padziko lonse lapansi
Kusamalira chiopsezo panthawi ya zilengezo zachuma
Kugwiritsa ntchito kalenda yachuma
- Yang'anani kalendayo tsiku lililonse, ndikuzindikira mlingo wa mphamvu ya chochitika chilichonse (chachikulu, chapakatikati, kapena chaching'ono).
- Yerekezerani ziwerengero zam'mbuyomu ndi zoneneratu.
- Yang'anirani mndandanda wa zilengezo zofunika zomwe zimatuluka nthawi imodzi.
Kuwongolera chiopsezo panthawi ya nkhani
Kusinthasintha kwa msika kumakwera kwambiri pakatuluka nkhani zazikulu. Nthawi zambiri ma Spreads amakula, ndipo kusinthasintha kwa mitengo kungakhale kosadziwika bwino. Ganizirani njira izi:
- Pewani kuchita malonda panthawi ya nkhani zazikulu pokhapokha ngati njira yanu ikugwirizana ndi kusinthasintha kwakukulu kwa msika.
- Kulitsani mlingo wanu wa Stop Loss kuti mupewe kutsekedwa kwa malonda anu mwachangu kwambiri.
- Chepetsani kukula kwa malonda kuti muwongolere chiopsezo.
Njira zodziwika bwino zochitira malonda panthawi ya nkhani
| Njira | Kachitidwe |
|---|---|
| Dikirani ndi Kuyang'ana | Lolani kuti kusinthasintha kwakukulu kwa msika kukhazikike musanalowe mumalonda. |
| Malonda Okonzedweratu | Konzani malonda molingana ndi kutuluka kwa deta yachuma yodziwika, pogwiritsa ntchito malo olowera ndi otulukira. |
| Malonda a Breakout | Lowani mumalonda mitengo ikadutsa pamlingo wofunikira pambuyo potuluka nkhani. |
Mfundo zofunika kuziganizira pa malonda a Forex
- Zizindikiro zachuma zosiyanasiyana zimakhala ndi mphamvu zosiyanasiyana pa ndalama.
- Momwe msika umachitira zimasiyana malinga ndi momwe chuma chilili.
- Kutuluka kwa deta zambiri nthawi imodzi kungabweretse zizindikiro zotsutsana.
- Momwe msika umayankhira sikuti nthawi zonse kumakhala komveka kapena kodziwika pasadakhale.
- Momwe msika unachitira m'mbuyomu sizitanthauza kuti udzachitanso chimodzimodzi mtsogolo.
Kuyamba kugwiritsa ntchito zizindikiro zachuma za Forex
- Tsatirani zizindikiro zazikulu monga GDP, ziwongoladzanja, ndi malipoti antchito.
- Yang'anirani momwe ma currency pairs omwe mwasankha amachitira pakatuluka nkhani.
- Sungani buku lolembera malonda anu kuti muzilemba momwe misika imayankhira pa deta yofunika yachuma.
- Yambani ndi malonda oyesera a demo musanagwiritse ntchito njira zanu pa malonda enieni.
Zizindikiro zachuma n'zofunika kwambiri kuti mumvetsetse kusuntha kwa msika, koma ndi gawo limodzi lokha la zinthu zonse. Amalonda ochita bwino amaphatikiza deta yachuma ndi kuwunika kwa ma chati komanso kasamalidwe kabwino ka chiopsezo.
Kulitsani kumvetsetsa kwanu pa Forex ndi maphunziro aulere pa maphunziro a Deriv Academy. Yeserani pa akaunti yoyesera malonda ya demo yaulere musanagwiritse ntchito nzeru zanu pa misika yeniyeni.
Lowani mu Deriv Academy pogwiritsa ntchito imelo ya akaunti yanu ya Deriv ndi mawu achinsinsi kuti muyambe.


