
Bitcoin siyifuna kufotokozedwa kwambiri. Ndi ndalama ya crypto yoyambirira, imene inayambitsa zonsezi. Koma dziko la crypto silinayimire pomwepo. Zikwizikwi za ndalama zatsopano zamakono zaoneka pa malonda a ndalama za crypto kuyambira pamenepo, iliyonse ikubweretsa chinthu chosiyana. Apa n'pamene pamabwera ma altcoin ndi ma stablecoin.
Tiyeni tifotokoze mwatsatanetsatane kuti n'chiyani komanso chifukwa chake zili zofunika.
Ma Altcoin: Opikisana nawo ambiri a Bitcoin
Ma Altcoin (mwachidule kuchokera pa 'alternative coins') amatanthauza ndalama za crypto zonse kupatulapo Bitcoin. Altcoin yoyamba inaoneka mu 2011, ndipo kuyambira pamenepo, opanga zinthu zamakono abweretsa zosintha ndi luso latsopano popanga ndalama zachitsulo zomwe zimagwira ntchito mwachangu, zotsika mtengo, komanso zosawononga mphamvu zambiri. Ma altcoin ena amagwira ntchito pa blockchain ya Bitcoin, pomwe ena, monga Ethereum, ali ndi maukonde awo apadera opangidwira zolinga zosiyanasiyana. Ganizirani za makontrakitala anzeru (smart contracts) ndi mapulogalamu osayendetsedwa ndi likulu limodzi.
Kodi mungachite malonda a ma Altcoin pa Deriv?
Inde ndithu! Amalonda ambiri amakonda ma altcoin chifukwa cha kusinthasintha kwawo kwamitengo. Kusinthasintha kwakukulu kwamitengo kungabweretse mwayi waukulu, koma pamodzi ndi chiopsezo chowonjezereka. Pa Deriv, simufunikira kugula kapena kukhala mwiniwake wa ma altcoin kuti muchite nawo malonda. Kaya mukuchita malonda a ma CFD kapena mukugwiritsa ntchito Multipliers, mukulospa za kusinthasintha kwa mitengo. Ngati zolosera zanu zili zolondola, mumapeza phindu popanda kuvutika ndi zikwama za ndalama zamakono kapena makiyi achinsinsi.
Inde, chiopsezo chikadalipobe pa malondawa. Njira yabwino yochitira malonda, zida zochepetsera chiopsezo monga Stop Loss, komanso kuwunika kolondola kwa msika zingakuthandizeni kukhala otetezeka.
Ma Stablecoin: Mbali yokhazikika ya crypto
Sizinthu zonse za ndalama za crypto zomwe mitengo yake imakwera ndi kutsika mwadzidzidzi. Ma stablecoin adapangidwa kuti azikhala okhazikika. Mtengo wawo umalumikizidwa ndi chuma monga dola ya ku America kapena golide, kawirikawiri pamlingo wa 1:1. Izi zikutanthauza kuti sakonda kusinthasintha mitengo mwadzidzidzi ndipo kawirikawiri amagwiritsidwa ntchito posinthana ndalama m'dziko la crypto.
Komabe, ma stablecoin sali opanda chiopsezo. Kugwa koopsa kwa Terra komwe kunatchuka mu 2022 kunatsimikizira kuti ngakhale chuma 'chokhazikika' chikhoza kutaya mtengo wake m'kamphindi. Choncho, ngakhale angakhale okhazikika kuposa Bitcoin kapena Ethereum, amabwerabe ndi ziopsezo zawozawo.
Kodi mungachite malonda a ma stablecoin pa Deriv?
Mungachite malonda a ma stablecoin pa Deriv, monga momwe mungachitire ndi ma altcoin. Popeza ma stablecoin sasintha mitengo mwadzidzidzi monga ndalama zina za crypto, sakhala oyenera kwenikweni pa malonda a tsiku ndi tsiku chifukwa cha kuchepa kwa kusinthasintha kwamitengo. Koma ngakhale kusintha kwakung'ono kwamitengo kungakhale kopindulitsa ngati mukuchita malonda ochuluka kapena ngati mumakonda kusinthasintha kochepa kwamitengo. Kuphatikiza apo, Deriv imakulolani kutsegula akaunti ya crypto pogwiritsa ntchito ma stablecoin, kuwapangitsa kukhala njira yothandiza pochita malonda m'misika ina nayonso.
Quiz
N'chiyani chimapangitsa ma stablecoin kukhala osiyana ndi ma altcoin?


